Malonje

Mu programu ya Malonje omvera amapereka malonje kwa abale ao, abwenzi, omwe amagwira nao ntchito , anthu omwe amawadziwa ndi ena ambiri. Timachezanso ndi akatswiri mu zigao zosiyana: nyimbo, ndale, zachilengedwe, uphunzitsi, ulimi ndi zina zambiri. Mkonzi wa programu ya lero ndi Ziyenela Zimba amene akucheza ndi oimba nyimbo zauzimu Elijah Sakala.